Mafunso Ndi Mayankho Vol. 4: Mau A Mulungu (Chichewa)

by Dana Dirksen

/
1.
2.
3.
4.
5.
6.
01:51
7.
8.
01:42
9.
01:45
10.
01:29
11.
12.
13.
14.
15.
16.

about

Mau a Mulungu ali ndi nyimbo zomwe zimathandizira kuphuzitsa Malamulo khumi a Mulungu komanso lamulo loposa ndi kufunikira kwakwe kwa izi. Nyimbo zina zoonjezera zikufotokoza m’mene mulungu anatipatsira ndi chifukwa chomwe anatipatsira Baibulo. Likufotokozanso chifukwa chomwe tiyenera kulikhulupilira komanso kuti ndilofunika bwanji kwa ife.
Zikomo

credits

released May 10, 2019

license

all rights reserved

tags

about

Songs for Saplings Portland, Oregon

We create lively, fun songs that attempt to deliver the deepest Biblical truths in a format that children will love.

Songs for Saplings is James and Dana Dirksen. We live in Portland, OR, and have 6 beautiful children. We thank God that He has allowed us to share the Good News that Jesus came to seek and save that which was lost.

You can learn more about us at songsforsaplings.com
... more

contact / help

Contact Songs for Saplings

Streaming and
Download help

Redeem code

Report this album or account

Track Name: Usakhale nayo Milungu ina koma ine ndekha
1. Usakhale nayo Milungu ina koma ine ndekha

Tsono Mose anatsika kuphiri
Kupita kwa anthu
Anachoka kuphiri anati Mulungu wanena izi kwa inu (*2)

Ndinakuchotsani m’dziko la iguputo dziko la ukapolo
Musakhale ndi milungu ina koma ine
Musakhale ndi milungu ina, ine ndekha

Tsono Mose anatsika kuphiri
Kupita kwa anthu
Anachoka kuphiri anati Mulungu wanena izi kwa inu

Mulungu wanena izi kwa inu
Mose anatsika, kutsika kuphiri
Ekisodo 20
Anatsika kuphiri anati
Mulungu wanena izi kwa inu
Track Name: Usadzipangire iwe wekha fano losema
2. Usadzipangire iwe wekha fano losema

Chifundo, chikondi
Ku zikwi zamibadwo
Za ondikonda
Chifundo, chikolndi
Ku zikwi zamibadwo za osunga malamulo
Usapange fanizo la chilichonse
Osagwada ndikulambira
Poti ndine Ambuye Mulungu wako
Mulungu wa nsanje
Olanga ana Kamba ka tchimo la kholo lawo
Kwa mibadwo ndi mibadwo ya ondida ine
Track Name: Usatchule dzina ya Yehova Mulungu wako pachabe
3. Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe

Oo mpatseni Ambuye, inu ana amphamvu
Ulemu ndi mphamvu kwa Yehova
Mpatseni Ambuye, dzina lake la ukulu
Dzina lake la ukulu mu mchiyero chake
Mlambireni

Oo liwu la yehova liri pa madzi
Ulemelero ugunda ku mapiri
Ulemelero ulu pamadzi onse
Oo Liu la Yehova lalikulu
Usatenge dzina la Ambuye pachabe
Muchiyero chake mlambireni
Mpatseni Ambuye
Dzina lake la ukulu
Masalimo 29:2
Mlambireni
Track Name: Tsiku la Sabata
4. Tsiku la Sabata

Tsono pali lasabata la anthu, la anthu a Mulungu
Poti Mulungu analenga kumwamba ndi dziko anapuma lasabata kuntchitozo
Iye opuma mwa Mulungu apuma mu zintchitozo
Yesetsani kupuma mwa iye kuti musagwe
Poti tili ndi wa msembe
Ali kwa iye, yesu mwana wa Mulungu
Tiyeni tigwiritse chikhulupiliro tili nacho
Anayesedwa ngati ife, opanda tchimo
Tifikere mpando wachisomo ndiungwiro
Kuti tilandire chifundo tikachifuna
Puma mwa Yesu, puma mwa Yesu
A heberi chaputala 4
Wansembe wathu mwana mwa Mulungu, mwana mwa Mulungu,
wamsembe wathu mwana wa Mulungu
Track Name: Lemekeza atate ako ndi amako
5. Lemekeza atate ako ndi amako

Ananu mverani makolo mwa Ambuye izi mzabwino
Lemekezani bambo ndi mayi
Ili ndi lamulo la lonjezo (*2)

Kuti zikuyendereni
mukhale ndi moyo wautali
Kuti zikuyendereni
Aefeso 6 vesi 1
Ananu mverani makolo mwa Ambuye izi Mzabwino
Lemekeza bambo ndi mayi
Ili ndi lamulo la lonjezo
Lemekeza bambo ndi mayi
Ili ndilamulo la lonjezo
Track Name: Usaphe
6. Usaphe
Tidziwa tachoka ku imfa
Chifukwa timakondana
Aliyense osakonda ali mu imfa
Aliyense oda mnzake waphwanya lamulo
Usaphe
Waphwanya lamulo
Usaphe
Ndi momwe tadziwira chikondi Yesu anatifelafe
Ndipo tiyenera kufera anzathu
1 Yohane 3:14
Kondanani
Track Name: Usachite dama
7. Usachite dama

Imwa madzi a mchitsime chako ndi mkasupe wako
Kodi magwero ako amwazike
M’mitsinje m’makwalala
Ikhale a iwe wekha
Osati ndi alendo okhala nawe

Kondwa ndi mkazi wako wa ubwana monga mbalawa
Yokondwa ndi chinkhoma cha chisomo
Miyambo 5:15 mpaka 19
Imwa madzi a chitsime ndi a kapuse wako
Usapange nawo zadama
Khala oyera m’tima, m’maganizo
Konda mwamuna wako
Khala oyera
Usapange nawo za dama
Khala oyera m’tima, m’maganizo
Konda mkazi wako khala oyera
Track Name: Usabe
8. Usabe

Iwe usabe, iwe usabe
Iwe wakuba usabeso
Usabeso kwa m’bale wako
Usabeso
Usabeso kwanzako onse
Usabeso

Iwe usabe, iwe usabe
Aefeso 4 vesi 28 usabeso
Koma ugwire ntchito mwachilungamo
Usabeso
Ndipo agawire kwa osowa
Usabeso
Track Name: Usaname
9. Usaname

Usaname Ambuye adana ndi onama (*3)
Koma akondwera mwa munthu
Oo Mbuye akondwera mwa munthu
Miyambo 12:22
Wachilungamo
Track Name: Usasilire
10. Usasilire

Khutitsidwa ndi zako
Khutitsidwa ndi zako
Khutitsidwa ndi zako
Khutitsidwa
Usasilire

Usasilire nyumba ya mzako
Usasilire mkazi wa m’nzako
Usasilire n’gombe ya m’nzako
Usasilire chilichonse chomwe ndi chamzako
Uuuuuu uuuuu uuuuuu
Mulungu anati
Simdza, simdza, simdzakusiya
Simdza, simdza, simdzakutaya
Simdza, simdza simdzakusiya
Simdza (*2)
Heberi 13 vesi 5 (*4)
Khutitsidwa
Track Name: Kodi tiphuzira kuti kukonda ndi kumvera Mulungu?
11. Kodi tiphuzira kuti kukonda ndi kumvera Mulungu?

Tiphunzira kuti kukonda?
Tiphunzira kuti kumvera Mulungu?
Tiphunzira kuti kukonda n’kumvera Mulungu?

Mu Baibulo tiphunzira kukonda
Mu Baibulo tiphunzira kumvera Mulungu
Mu Baibulo tiphunzira kukonda n’kumvera Mulungu

Sunga buku lachilamulo pakamwa pako
Liwerenge tsiku ndi tsiku
Kuti usamale mkuchita zonse zolembedwamo
Yoswa chaputala 1 vesi 8
Track Name: Analemba Baibulo ndi ndani?
12. Analemba Baibulo ndi ndani?

Mzakukumbutsani nthawi zones za izi
Ndingakhale m’dziwe muli mchilungamo
Muli maso koma mdzakupatsani kupeza kwa bwino
Kukupatsa mpaka kuchoka msasa omwe ndili nawowo
Uuuuuuuuu uuuuuuuuu uuuuuuuwaaaaa
Ndipo mumvetsere bwino za izi mpaka kuwala mu mdima
Kuwala mu mdima
Ndipo inu mumvetsere bwino za izi mpaka kuwala kwa mawa
Mpaka nyali iwale mu mitima yanu
Uuuuuuuuuuu uuuuuuuu uuuuuuwaaa
Analemba Baibulo anthu a Mulungu
Osankhidwa ndi Mulungu
Analemba Baibulo anthu a Mulungu
Owuzidwa ndi Mzimu oyera
2 Petro 1
Anthu analankula
Monga mwa mzimu oyera
Track Name: Kodi lamulo la likulu ndi liti?
13. Kodi lamulo la likulu ndi liti?

Phuzitseni lamulo lalikulu mchani?
Konda Mulungu ndi mtima, moyo n’zeru zako
Phuzitseni lamulo lalikulu n’chani
Konda m’nzako ndi lamulo la chiwiri (*2)

Konda Ambuye Mulungu
Ndi mtima wako
Konda Ambuye Mulungu
Ndi moyo wako
Konda Ambuye mulungu
Ndi nzeru zako
Kondaso mzako ndi mtima onse
Chiphatikizo chonse
Mateyu 22 ndime 36
Chiphatikizo chonse
Track Name: Kodi Mulungu amakondwela ndi omukonda komanso omumvera?
14. Kodi Mulungu amakondwela ndi omukonda komanso omumvera?

Ndikonda ondikonda
Ndipo ondifuna adzandipeza
Ndikonda ondikonda
Miyambo 8 vesi 17 (*2)

Iye osunga malamulo anga
Ndiye ondikonda, ndiye ondikonda
Adzakondedwa ndi atate anga
Ndiye ondikonda, ndiye ondikonda
Ndidzakondanso, ndizakonda
Amakondanso amakonda
Ndidzazionetsera kwa iye
Ndiye okonda

Ndikonda ondikonda
Ndipo ondifuna adzandipeza
Ndikonda ondikonda
Miyambo 8 vesi 17

Iye osunga malamulo anga
Ndiye ondikonda, ndiye ondikonda
Adzakondedwa ndi Atate anga
Ndiye ondikonda, ndiye ondikonda
Mulungu akondwa omukonda ndi omvera?
Amakondanso omukonda
Yohane 14 vesi 21
Ndiye ondikonda
Track Name: Kodi Mulungu sakondwela ndi omuda komanso osamumvera?
15. Kodi Mulungu sakondwela ndi omuda komanso osamumvera?

Masalimo chaputala 7:9 mpaka 11(*2)
Atate wa mwamba odziwa iso ndi mtima
Thetsani nkhondo zaoipa nditetezeni
Chida changa ndinu
Mupulumutsa oongoka, oweruza wangwiro
Mumva mkwiyo nthawi zones
Oooooh owuhooooo hoooo
Mulungu sakondwera ndi omuda iye
Amakwiya ndi woipa nthawi zonse
Mulungu sakondwera ndi osamvera?
Amakwiya ndi woipa nthawi zonse
Musang’ambe zovala zanu muchisoni
Koma mitima, bwererani kwa Ambuye
Ngwachifundo, chikondi, wosakwiya nsanga
Ngokhululuka, ali chile kuleza
Yoweli 2:13
Track Name: Kodi malamulo khumi ndi antchito yanji?
16. Kodi malamulo khumi ndi antchito yanji?

Chani? Bwanji?, ndiyese? Zabwino bwanji?
Zabwino bwanji kwa ine?(*2)
Kuti zindiphuzitse ntchito, kwa anthu ndi kwa Mulungu okhala oyera
Monga Mulungu
Deturonome 29
Zodziwika kwa ife ndi ana athu mpaka kale

Chani? Bwanji?, ndiyese? Zabwino bwanji?
Zabwino bwanji kwa ine? (*2)
kuti zionetse kufuna kwathu ife
Tifunitsa mpulumutsi, mpulumutsi
Kuti titsate chilamulo
Deturonomo 29:29