Mafunso Ndi Mayankho Vol. 3: Khristu Ndi Ntchito Zake (Chichewa)

by Dana Dirksen

/
1.
2.
3.
4.
5.
6.
7.
8.
9.
10.
11.
12.

about

“Khristu ndi ntchito zake” ikufotokoza chifukwa chimene Mulungu anatuma Yesu. Ntchito imene Yesu adagwira kukwanilitsa chipulumutso chathu ndi zimene akuchitabe mpakana lero. Nyimbozi zikuphuzitsa zoona zokhazokha kuchokera mmau a Mulungu za chikhalidwe cha Yesu, ntchito zake (mu ufumu wa Mulungu) komanso m’mene anatilumikizitsira ndi Mulungu.
Zikomo

credits

released May 10, 2019

license

all rights reserved

tags

about

Songs for Saplings Portland, Oregon

We create lively, fun songs that attempt to deliver the deepest Biblical truths in a format that children will love.

Songs for Saplings is James and Dana Dirksen. We live in Portland, OR, and have 6 beautiful children. We thank God that He has allowed us to share the Good News that Jesus came to seek and save that which was lost.

You can learn more about us at songsforsaplings.com
... more

contact / help

Contact Songs for Saplings

Streaming and
Download help

Redeem code

Report this album or account

Track Name: Ungalape ndi kukhukhulupilira Khristu ndi mphamvu zako?
1. Ungalape ndi kukhukhulupilira Khristu ndi mphamvu zako?

Maso anu sanaone makutu sanamve
Palibe amadziwa zomwe Mulungu wakonza
Kwa iwo womkonda
Mulungu wazionetsa kwa ine (*2)

Ungalape ndi kukhulupira Khristu
Ungalape ndi kukhulupira ndi mphamvu zako ungakhulupilire
Mulungu wazionetsa kwa ine

Sitinalandire, mzimu wamdziko
Koma mzimu wa kwa Mulungu
Kuti tidziwe ndikumvetsa zomwe Mulungu watipatsa
Mulungu wandipatsa ulele

1 Akolinto, chaputa 2 ndime 9
Palibe amadziwa zomwe Mulungu wakonza
Kwa iwo omkonda
Mulungu wazionetsa kwa ine
Ayi sinadziwe za chipulumutso changa koma Khristu wazionetsa izi kwa ine
Track Name: Kodi chiyanjano ndi chain?
2. Kodi chiyanjano ndi chani?

Na na na na na na na na na na (*4)
Chiyanjano
Kodi chiyanjano ndi chani
Chiyanjano
Kodi chiyanjano ndi chani
Na na na na na na na na na na

Tapulumutsidwa kumkwiyo wa Mulungu
Mwa mwana wake
Na na na na na na na na na
Chikondi chinaoneka tikadali ochimwa
Tili ochimwa Khristu adatifera
Na na na na na na na na na

Khristu anasangalatsa Mulungu potifera ife mwalo mwathu
Sangalalani mu ubale wa ife ndi Mulungu (*2)
Aroma 5:8 mpaka 11
Sangalalani mu ubale wa ife ndi Mulungu (*2)
Na na na na na na na na na
Track Name: Kodi anthu amapulumuka bwanji Khristu asanabwere?
3. Kodi anthu amapulumuka bwanji Khristu asanabwere?

Abelo enoki, Nowa , Abrahamu, Isake, Yakobo, Sara, Yosefe
Makolo a mose, Mose, Lahabe, Gidioni, Barati, Samisoni, Yefita
Davide, Samueli ndi Aneneri

Kuyang’anira ku mzinda
Kufunitsitsa kumwamba

Anthu onsewa anali mchikhulupiliro pakufa
Sanalandire zolonjezedwa, anangoziona patali
Anangoona ndi kuzilandira patali
Kufunitsa ku mwamba

Anthu ankapulumuka bwanji Khristu asanabwere
amkapulumuka pokhulupira
Kukhulupira mpulumutsi
Heberi 11
Kukhulupira mpulumutsi
Track Name: Kodi anthu amawonetsa bwanji chikhulupiliro Khristu asanabwere?
4. Kodi anthu amawonetsa bwanji chikhulupiliro Khristu asanabwere?

Mchikhulupiro Abelo anapeleka nsembe yabwino kuposa Kaini
Iye anatengedwe wangwiro
Mulungu anamuyamikira

Chikhululukiro chinalipo bwanji Khristu asanabwere
Chimkaoneka popeleka nsembe
Yomwe mulungu analamula

Msembeyi ikuimira ndani
Khristu mwana wa nkhosa
Khristu mwana wa nkhosa
Wofera machimo a mdziko

Onani mwana wankhosa ochotsa machimo a mdziko
Yohane 1:29
A Heberi 11 vesi 4
Onani mwana wa Nkhosa ochotsa machismo mdziko
Yohane 1:29
Khristu mwana wankhosa wachotsa machimo mdziko
Track Name: Kodi Khristu anakhala bwanji munthu, popeza iye ndi Mulungu mwana?
5. Kodi Khristu anakhala bwanji munthu, popeza iye ndi Mulungu mwana?

Maria usaope
Wapeza chisomo ndi Mulungu
Udzakhala ndi pakati nudzabala mwana wa mmuna
Udzamutcha dzina lake Yesu (*2)

Adzakhala wamkulu
Adzatchulidwa mwana wa wamkulu (*2)
Adzakhala wamkulu
Adzatchulidwa mwana wamkulu (*2)

Ambuye adzampatsa ufumu wa Davite
Adzalamulira nyumba ya Yakobo
Ufumu wake sudzatha
Ufumu wake sudzatha
Maria usaope wapeza chisomo ndi Mulungu

Kodi Khristu anakhala bwanji Munthu?
Iye ponga Mulungu anakhala munthu pobadwa
Ndi mphamvu ya mzimu woyera ndi thupi ndi moyo
Mu mmimba mwanamwali Maria
Luka 1:20 mpaka 33
Maria
Track Name: Kodi Yesu anachimwako?
6. Kodi Yesu anachimwako?

2:22, I petro 2:22
Sanachimwe, sanachimwe
M’mau ake munalibe chinyengo konse

Kodi Yesu anachimwa?
Ayi!
Yesu anali wamgwiro
Track Name: Kodi Yesu anafa imfa yotani?
7. Kodi Yesu anafa imfa yotani?

Usadzikonde, Usadzitame
Usaganize ndiwe ndiwe oposa onse
Samala za ena osati iwe wekha
Maganizo a Khristu khale mwa iwe

Maganizo a Khristu akhale mwa iwe
Okhala Mulungu mchilengedwe chake
Ponga Mulungu sanachiyese, cholanda

Khristu anadzichepetsa
Anakhala kapolo
Kubadwa monga munthu
Anakhala kapolo

Infa yotani Khristu anafa
Imfa yowawa pamtanda
Afilipi chaputala 2
Imfa ya manyazi

Mulungu anamukweluza
Kumpatsa dzina loposa onse
Bondo ligwande, kamwa livomereza Khristu ndi Ambuye (*2)

Ulemu kwa Mulungu, Ulemu kwa Atate
Track Name: Kodi ndi ntchito zanji Khristu anachita monga Mesiya olonjezedwa?
8. Kodi ndi ntchito zanji Khristu anachita monga Mesiya olonjezedwa?

Ntchito zanji Khristu anachita
Monga Mesiya olonjezedwa
Mneneri, Mbusa, mfumu

Kwa ife, mwana wabadwa
Mwana wa mamuna wapatsidwa
Ndi ulamuliro uli pa phewa lache
Adzatchedwa waumphungu odabwitsa
Mulungu wamkulu , Tate wosatha
Kalonga wa mtendere
Tutu tulututu (*2)

Ntichito zanji Khristu anachita
Monga Mesiya olonjezedwa
Mneneri, M’busa, Mfumu

Yesaya vesi 6 chaputa 9
Kwaife mwana wapatsidwa
Ndi ulamuliro uli pa phewa lache
Adzatchedwa waumphungu odabwitsa
Mulungu wamkulu Tate osatha
Kalonga wa mtendere
Track Name: Kodi Khristu akhala bwanji Mneneri wako?
9. Kodi Khristu akhala bwanji Mneneri wako?

Ndiphuzira chifuniro chake
Khristu andiphuzitsa chifuniro chake

Kuchoka mbuku la Yesaya 61 Khristu anawelenga
Mzimu wa Ambuye uli pa ine
Pakuti wandidzodza ndilalikire kwa osauka
Kumasula a msinga
Osaona kuti aone
Kulimbikitsa ofooka
Kukhazikitsa chaka chokomera Yehova

Ndiphuzira chifuniro chake
Khristu andiphuzitsa chifuniro chake

Khristu ali bwanji mneneri
Yohane 15 :15
Ndiphuzira chifuniro chake
Khristu andiphuzitsa chifuniro chake
Zonse ndaphuzira kwa a tate ndakudziwitsani
Mzimu wa Ambuye ali pa ine
Pakuti wandidzodza ndilalikire kwa osauka
Kumasula msinga
Track Name: Kodi Khristu akhala bwanji wamsembe wako?
10. Kodi Khristu akhala bwanji wamsembe wako?

Khristu ndi m’busa bwanji
Anandifera
Khristu ndi m’busa bwanji
Andipemphelera
Anatsuka machimo anga onse
Anatsuka machimo anga onse andipemphelera

Akwanilitsa kwa a muyaya
Kupulumutsa obwera kwa Mulungu mwa iye (*2)

Aheberi 7 vesi 25 andipemphelera (*2)
Track Name: Kodi Khristu akhala bwanji mfumu yako?
11. Kodi Khristu akhala bwanji mfumu yako?

Khristu ali mfumu bwanji?
Khristu, olamula, ateteza
Akhazikitsa ufumu wake mdziko

Khristu ali mfumu bwanji?

Mbuye woweluza
Mbuye wolamula
Ndiye wopulumutsa
Mbuye ndi mfumu
Mbuye ndowoweruza
Mbuye ndi mfumu
Yesaya 33 ndime 22
Track Name: Kodi ungalape ndi kukhulupilira Khristu ndi mphamvu zako?
12. Kodi ungalape ndi kukhulupilira Khristu ndi mphamvu zako?

Ungalape?
Ungakhulupilire?
Ungalape ndukhulupilira Khristu ndi mphamvu zako? (*2)
Maso sanawone, makutu sanamve
Palibe amadziwa zomwe Mulungu wakonza kwa iwo womkonda
Mulungu wazionetsa kwa ine
Ndi mzimu wake wazionetsa kwa ine
Ndingalape
Ndingakhulupilire
Ndingalape ndikukhulupilira Khristu ndi Mphamvu yako

Sitinalandire mzimu wamdziko koma mzimu wa kwa Mulungu
Kuti tikamvetse zomwe Mulungu watipatsa ulere
Wandipatsa ulere
1 Akolinto 2
Wandipatsa ulere
Ungalape?
Ungakhulupilire