Mafunso ndi Mayankho Vol. 2: KUGWA NDI CHIPULUMUTSO (Chichewa)

by Dana Dirksen

/
1.
2.
3.
4.
5.
6.
7.
8.
9.
10.
11.
12.
13.
14.
15.
16.
17.
18.
19.
20.
21.
22.
23.
24.
25.
26.
27.
28.
29.
30.

credits

released January 1, 2015

license

all rights reserved

tags

about

Songs for Saplings Portland, Oregon

We create lively, fun songs that attempt to deliver the deepest Biblical truths in a format that children will love.

Songs for Saplings is James and Dana Dirksen. We live in Portland, OR, and have 6 beautiful children. We thank God that He has allowed us to share the Good News that Jesus came to seek and save that which was lost.

You can learn more about us at songsforsaplings.com
... more

contact / help

Contact Songs for Saplings

Streaming and
Download help

Redeem code

Report this album or account

Track Name: CHIPANGANO NDI CHANI?
1. CHIPANGANO NDI CHANI?

Ndi Ambuye ndi Ambuye
Ndi Ambuye Mulungu wathu

Maweruzo ake ali padziko
Akumbukira chipangano kwa muyaya
Mau anawalamulira, mibadwo zikwi
(Masalimo 105: 7 ndi 8)
 
Ndi Ambuye ndi Ambuye
Mulungu wathu
 
Chipangano ndi chiani?
Mgwirizano Mulungu apanganafe
Omwe atsimikiza kusunga
Kusunga Lonjezo Lake
Kusunga Lonjezo Lake
Track Name: GAWO LA ADAM MU CHIPANGANO KUTI AKHALEBE MMUNDA WA EDENI NLITI?
2. GAWO LA ADAM MU CHIPANGANO KUTI AKHALEBE MMUNDA WA EDENI NLITI?

Gawo la Adamu muchipangano
Kuti akhalabe mmunda wa Edini nliti
Adamu ayenera kumvera Mlungu wangwiro

Ndipo Yehova anati kwa munthu
Mitengo yonse ya mmundayo udye
Koma usadye mtengo wakudziwitsa zabwino ndi zoipa

Usadye mtengo wakudziwitsa zabwino ndizoipa
Chifukwa ukadya udzafa ndithu
(Genesis 2: 15 mpaka 17)
Track Name: KODI ADAMU ADAMVERA MULUNG?
3. KODI ADAMU ADAMVERA MULUNG?

Kodi Adamu adamvera Mulungu?
Ayi Adamu adasankha kusamvera Mlungu
Adamu adasankha kusamvera
 
Mmene mkazi anaona chipatso
Chinali chabwino kudya, chokongola m’maso
Chipatso cholakalakika kupatsa nzeru
Anatenga chipatso nadya napatsa
Mwamuna anali naye nadya
(Genesisi 3 ndime 6)
Adamu anasankha kusamvera
Track Name: MULUNGU ANALANGA KUSAMVERA KWA ADAMU MOTANI?
4. MULUNGU ANALANGA KUSAMVERA KWA ADAMU MOTANI?

Minga, zilonda ndi minga, zilonda ndi minga
Zilonda yotembereredwa nthaka
Minga, zilonda ndi minga, zilonda ndi minga,
Zilonda masiku a moyo wonse
 
Zowawa, zokhoma, zowawa, zokhoma
Zowawa zokhoma udzadya m’menemo
Zowawa zokhoma zowawa zokhoma
Zowawa masiku a moyo onse

Kuchotsedwa m’munda wa Edeni
Kugwira ntchito mnthaka yomwe anachokera
Kupirikitsidwa m’munda wa Edeni
Olondedwa ndi lupanga la moto
Mulungu analanga kusamvera kwa Adamu motani?
Chilango cha Adamu chinali
Imfa ndi kulekana ndi Mulungu
(Genesisi 3 ndime 17 mpaka 24)
Track Name: TCHIMO NDI CHANI?
5. TCHIMO NDI CHANI?

Chifundo chanu,
Kumbukirani nsoni zanu Mbuye, Kukoma mtima kwanu
Chifundo chanu, pakuti izi
Nzakale lonse, chifundo ndi chikondi chanu
Musakumbukire zolakwa za ubwananga
zopikisana nanu
Mundikumbukire monga mwa chifundo chanu
Chifukwa chaubwino wanu
Tchimo ndi chani?
Tchimo ndi kusamvera chilamulo cha Mulungu,
Polephera kupanga zotilamulira
Kapena kupapanga zoletsedwa ndi Mulungu
(Masalimo 25 ndime 6 ndi 7)
Chifundo chanu
Track Name: SATANA NDI NDANI?
6. SATANA NDI NDANI?

Dziletseni dziletseni dziletseni dikirani
Dziletseni dziletseni dziletseni dikirani

M’dani wanu Satana ayenda ngati mkango
Kufuna womulikwira
 
Satana ndi ndani?
Satana ndi mzimu woyipa
Wodana ndi Mulungu ndi Akhristu
(1 Petro 5 ndime 8)
Dziletseni dikilani
Track Name: WAMKULU NDANI MULUNGU NDI SATANA?
7. WAMKULU NDANI MULUNGU NDI SATANA?

Wamkulu ndi ali mwa inu
Kuposa ali m’dziko
 
Wamphamvu ndani Mulungu kapena Satana?
Mulungu ndiye wamphamvu
Ndinu ochokera kwa Mulungu
Mwapambana iwo a mdziko
(1 Yohane 4:4)
Track Name: KODI TCHIMO LA MAKOLO ATHU OYAMBA NDI LITI?
8. KODI TCHIMO LA MAKOLO ATHU OYAMBA NDI LITI?

Gene Gene Gene Genesis 3 vesi 6
Gene Gene Gene Genesis 3 vesi 6
munthu anachimwa pa
Genesisi 3 vesi 6

Tchimo lamakolo oyamba nliti?
Kudya chipatso choletsedwa
Kudya chipatso choletsed
Track Name: ANAMUYESA ADAMU NDI HAVA KUTI ACHIMWE NDI NDANI?
9. ANAMUYESA ADAMU NDI HAVA KUTI ACHIMWE NDI NDANI?

Anamuyesa Hava? Anamuyesa Adamu ?
Anamuyesa Adamu ndi Hava ndani?
Satana anayesa Hava
Nampatsa chipatso adamu
Adamu chipatso na chidya
 
Pa Genesis 3
Njoka inati kwa mkazi
Simudzafa yi Mulungu adziwa
maso anu adzatsekuka
Mudzakhala ngati Mulungu,
Wodziwa zabwino ndi zoipa
Mudzakhala ngati Mulungu
Track Name: CHINACHITIKA NCHIYANI KWA ADAMU NDI HAVA ATACHIMWA?
10. CHINACHITIKA NCHIYANI KWA ADAMU NDI HAVA ATACHIMWA?

Chinachitika n’chiani kwa Adamu ndi Hava atachimwa?
M’malo mokhala oyera ndi okondwa
Anakhala ochimwa ndi ovutika

Odziwa zabwino ndizoyipa
Genesisi 3:22
Zabwino ndi zoipa
Track Name: KODI TCHIMO LA ADAMU LINAKUTANI?
11. KODI TCHIMO LA ADAMU LINAKUTANI?

Tchimo la adamu linakuta ni
Linandipanga womanyazi ndi wochimwa
Monga mmene tchimo linalowela mdziko
Mwa munthu, imfa mwa tchimo
Momwemonso imfa inabwera kwa munthu
Chifukwa cha tchimo
na na na na na na na n
Imfa ndi Adam moyo ndi Khristu
Aroma 5:12
Track Name: KODI TCHIMO LILILONSE LITITENGERA CHIYANI?
12. KODI TCHIMO LILILONSE LITITENGERA CHIYANI?

Tchimo litlitengera chiyani?
Mkwiyo wa Mulungu
Temberero la Mlungu
 
Ana akataya chilamulo
Osayenda m’maweruzo anga
Nakaipsa malemba anga osasunga malamulo,
Ndidzalanga tchimo lawo
Masalimo 89 ndime 30 mpaka 32
Track Name: KODI NDIWE OCHIMWA MOTANI MWACHIKHALIDWE?
13. KODI NDIWE OCHIMWA MOTANI MWACHIKHALIDWE?

Palibe mmodzi
Palibe inde ngakhale m’modzi
Palibe oyera
Palibe mmodzi
Palibe amene amvetsetsa
Afuna Mulungu
Palibe mmodzi
Apatuka alowerera
Palibe m’modzi wochita zabwino, olo m’modzi
Ochimwa mwachibadwe
Palibe oyera
Ndiwe woipitsitsa mmagawo onse
Afuna Mulungu
Palibe
Aroma 3 ndime 11 mpaka 12
Palibe m’modzi wochita zabwino, olo m’modzi
Track Name: KODI UNGAPITE KCHUMWAMBA NDI CHIKHALIDWE CHA UCHIMO?
14. KODI UNGAPITE KCHUMWAMBA NDI CHIKHALIDWE CHA UCHIMO?

Mulungu anakonda dziko lapansi
Nanapatsa mwana wake yekhayo
Kuti onse okhulupirira Iye
Asatayike akhale nawo moyo

Ungapite kumwamba ndi chikhalidwe cha uchimo?
Ayi mtima uyenera kusinthka
Mtima wanga usinthe ndisanapite kumwamba.
Yohane 3:16
Track Name: KODI KUSINTHA KWA MTIMA KUTCHEDWA CHIYANI?
15. KODI KUSINTHA KWA MTIMA KUTCHEDWA CHIYANI?

Ezekiyele 36: 26 mpaka 27
Mdzakupatsa mtima watsopano
Mkati mwanu Mzimu watsopano
M’dzachotsa mtima wa mwala
Kukupatsani mtima wa mnofu
Kukupatsani Mzimu wanga
Kukuyendetsa m’malemba anga
Mudzasunga maweruzo anga
Ndikuwachita malemba anga
Kusintha mtima mchani?
Kusintha mtima kutchedwa kubadwanso
Kusintha kwa mtima mmchani?
Kutchedwa kubadwanso
Ezekiele 36
 
Track Name: ANGASINTHE MTIMA WA OCHIMWA NDANI?
16. ANGASINTHE MTIMA WA OCHIMWA NDANI?

Palibe mpulumutsi winanso
Palibe dzina lina pansi pathambo
Lopatsidwa, kwa anthu kupulumutsa
lnde palibe dzina lina

Angasinthe mtima ndani?
Mulungu yekha Mulungu yekha
Mulungu yekha angasinthe mtima ochimwa
Machitidwe 4 ndime 12
Palibe dzina lopatsidwa kwa anthu
Limene lipulumutsa.
 
Track Name: MPULUMUTSI WA OSANKHIDWA A MULUNGU NDI NDANI?
17. MPULUMUTSI WA OSANKHIDWA A MULUNGU NDI NDANI?

Ndani ndani ndani mpulumutsi
Mpulumutsi wa osankhidwa a Mulungu
Ndani ndani ndani mpulumutsi
Mpulumutsi waosankhidwa a Mulungu

Yekhayo mpulumutsi ndiye Yesu Khristu
Mwana wa muyaya wa Mulungu
Anakhala munthu, komanso ali Mlungu
Munthu m’modzi zilengedwe ziwiri

Ndine njira, choonadi ndi moyo
Palibe adza kwa Atate osadzera mwa Ine
Ine ndi njira, choonadi ndi moyo
Yohane 14 ndime 6
 
Track Name: MTIMA WAKO USINTHA BWANJI?
18. MTIMA WAKO USINTHA BWANJI?

Mtima usintha bwanji?
Mtima wanga usintha ndi Mzimu Woyera
Mtima usintha bwanji?
Mchisomo cha Mulungu
Mtima usintha bwanji?
Chooneka mntchito ya Khristu
Mtima wasintha mchisomo cha Mulungu
 
Chifundo chikondi cha Mulungu zidaoneka
Mpulumutsi wathu
Adapulumutsa osachokera muntchito
Mwachifundo chake
Kupulumutsa mwakutsuka kwa kubadwanso
Ndi makonzedwe a Mzimu Woyera
Amene apereka mochurukira
Khristu Mpulumutsi wathu
Tito mutu 3 ndime 4, 5 ndi 6
Track Name: CHISOMO NDI CHIYANI?
19. CHISOMO NDI CHIYANI?

Ndinu anthu wopatulika wa Mulungu
Ambuye Mlungu wakusankhani
Ndinu mtundu wa wopatulika wa Mulungu
Wosankhidwa kuchokera mdziko
Chisomo mchani?
Chisomo ndi chifundo cha cha Mulungu
Poyenera chilango
Deuteronomo 7 ndime 6
Track Name: KHRISTU ADAGWIRA NTCHITO YANJI YOKUPULUMUTSA?
20. KHRISTU ADAGWIRA NTCHITO YANJI YOKUPULUMUTSA?

Mulungu anamuyesa, iye
Wopanda uchimo kukhala tchimo
Kukhala tchimo m’malo mwathu
Kuti mwa iye tikakhale tikakhale
Chiyero cha Mulungu
Chiyero cha Mulungu
2 Akorinto 5 ndime 21

Khristu adatani populumutsa?
Adasunga malamulo a Mulungu
Nalangidwa chifukwa cha machimo anga
Chifukwa cha machimo anga
Track Name: ALIPO ANGAPULUMUTSIDWE NDI NTCHITO ZAKE?
21. ALIPO ANGAPULUMUTSIDWE NDI NTCHITO ZAKE?

Angapulumuke ndani ndi tchito zake
Palibe angapulumutsidwe
Ndimwachisiomo mwapulumuka
Pokhulupilira osati nokha
Iyi ndi mphatso ya Mulungu
Aefeso 2 ndime 8
Iyi ndi mphatso yokongola
 
Track Name: TIPINDULANJI KU NTCHITO YA CHRISTU?
22. TIPINDULANJI KU NTCHITO YA CHRISTU?

Tipindulanji ku ntchito ya Khristu?
Mlungu akonzanso, ayeretsa
Mlungu akozanso, ayeretsa
Alungamitsa okhulupira Khristu
Munasambitsidwa munayeretsedwa
Munalungamitsidwa mdzina
Mdzina la Ambuye Yesu
Christu mwa Mzimu wa Mulungu
1 Akorinto 6 ndime 11
Mulungu, akonzanso ayeretsa
1 Akorinto 6 ndime 11
Ayeretsa okhulupira Khristu.
Track Name: KULUNGAMA NDI CHANI?
23. KULUNGAMA NDI CHANI?

Kulungama ndi chiyani?
Kulungama ndipamene Mulungu akhululukira
machimo onse kundipanga wangwiro
Choncho palibe kutsutsidwa
Onse ali mwa Yesu Khristu
Aroma Mutu 8 ndime 1
 
Track Name: UNALUNGAMITSIDWA BWANJI?
24. UNALUNGAMITSIDWA BWANJI?

Lungamitsiwa, lungamitsiwa lungamitsiwa
Ndalungama, lungamitsidwa, lungamitsidwa
Munchito ya Khristu 

Chifukwa cha chiyero
Chifukwa chachiyero
 
Ulungama bwanji?
Munthu sayesedwa olungama
Pantchito ya malamulo
Koma mwa chikhululupiriro cha Yesu.
Agalatiaya 2 ndime 6
 
Track Name: KUYERETSEDWA NDI CHANI?
25. KUYERETSEDWA NDI CHANI?

Kuyeretsedwa ndi chiyani?
Kuyeretsedwa Mulungu kundipanga wangwiro
Mtima ndi khalidwe
Kundiyeretsa
 
Mulungu wamtendere ayeretse konseko
Mzimu, moyo ndi thupi lanu
Zisungidwe za mphumphu.
Pakubwera Ambuye wathu Yesu Khristu
Wakuyitana ngokhulupirika
Mlungu adzazichita
1 Atesolonika 5:23 ndi 24
Wokwiyitana ngokhulupilika
Mlungu adzazichita
Track Name: MAGAWO AWIRI A CHIYERO NDI ATI?
26. MAGAWO AWIRI A CHIYERO NDI ATI?

Kufa kuuchimo moyo mchiyero
Kufa kuuchimo moyo mchiyero
Kufa kuuchimo moyo mchiyero
Magawo awiri achiyero ndi cha?
Ndinapachikidwa ndi Khristu sindiri wa moyo
Khristu akhala mkati mwanga
Moyo wanga mthupirili ndi mwachikhulupiro mwa Khristu
Nandikonda nadzipereka kwa ine
Agalatiya 2 ndime 20
Ndikhala mchikhulupiriro
Nandikonda nadzipereka ine
Nandikonda nadzipereka ine
 
Track Name: KODI KHRISTU ADAFERA NDANI?
27. KODI KHRISTU ADAFERA NDANI?

Simukhulupirira chifukwa, sinu nkhosa zanga
Nkhosa zanga zimandivera
Ndizidziwa, zinditsata
Ndipo sizidzaonongeka
Palibe wozikwatula m’dzanja langa
Atate wanga wondipatsa izo ,ndi wamkulu pa onse
Yohane 10 ndime 26 mpaka 29
Palibe adzazikwatula
Khristu adafera nda?
Adafera onse, opatsidwa kwa Iye ndi Atate
 
Track Name: ADZAPULUMUTSIDWE NDIYANI?
28. ADZAPULUMUTSIDWE NDIYANI?

Woyipa asiye njira yake
Wosalungama maganizo ake
Nabwere nabwere kwa Ambuye
Adzamchitira chifundo iye
Adzamchitira chifundo iye
Awererani kwa Mbeye, pakuti adzakhululukira
Adzamchitira chifundo
Yesaya 55 ndime 7
Adzapulumuka ndini?
Yense olapa ndikukhulupirira
Wokhulupirira Ambuye Yesu Khristu
 
Track Name: KODI KULAPA NDI CHIYANI?
29. KODI KULAPA NDI CHIYANI?

Kodi kulapa ndi chiyani?
Kulapa ndi kumva chisoni
Chifukwa cha tchimo, kudana nalo ndikulisiya
Chifukwa silikondweretsa Mulungu
Anthu anga otchulidwa ndi dzina langa
Akadzichepetsa mkupemphera
Nakafuna nkhope yanga nasiya njira zoyipa
Ndidzamvera ndikukhululukira
Mbiri 7: 14
 
Track Name: CHIKHULUPILIRO MWA KHRISTU NDI CHANI?
30. CHIKHULUPILIRO MWA KHRISTU NDI CHANI?

Chikhulupiro mchiyani?
Kukhulupilira Khristu
Chikukhulupiliro ndikudalira Yesu yekhayo pachipulumutso
Chikhulupiliro mchani
Kukhulupilira Khristu
Chikhulupiliro ndikudalira Yesu yekhayo
Afilipi 3 ndime 9
Chiyero chochokera kwa Mulungu
Pokhulupilira Khristu
Wosakhala chiyero changa
Chochokera mu lamulo
Chomwe chili po khulupilira Khristu