Mafunso ndi Mayankho Vol. 1: Mulungu ndi Chilengedwe (Chichewa)

by Dana Dirksen

/
1.
2.
3.
4.
5.
6.
7.
8.
9.
10.
11.
12.
13.
14.
15.
16.
17.
18.
19.
20.
21.
22.

about

Find out how you can help support our ongoing work in Malawi by visiting songsforsaplings.com/missions/chichewa

This is the Chichewa version of "Questions with Answers Vol. 1: God and Creation"

credits

released October 10, 2010

Singers:
Linda Chiyani
Levi Dannayo
Gerald Chimkoka

Numeri Mwale
Calrorine Mwale

Michelle Chipingu
Jerush Chipingu

African Drums:
Levi Dannayo

Recording Engineer:
Matthew H. Curl

Place of recording:
African Bible College in Malawi

songsforsaplings.com/missions/chichewa

license

all rights reserved

tags

about

Songs for Saplings Portland, Oregon

We create lively, fun songs that attempt to deliver the deepest Biblical truths in a format that children will love.

Songs for Saplings is James and Dana Dirksen. We live in Portland, OR, and have 6 beautiful children. We thank God that He has allowed us to share the Good News that Jesus came to seek and save that which was lost.

You can learn more about us at songsforsaplings.com
... more

contact / help

Contact Songs for Saplings

Streaming and
Download help

Redeem code

Report this album or account

Track Name: MLUNGU NDI NDANI?
1. MLUNGU NDI NDANI?

Mlungu ndi ndani?
Mlungu ali yekhayo, wamoyo oona
Ndiwaulemerero, wamphamvu amadziwa
zonse,
Namalenga wamkulu, ndi mbuye, wadziko—lonse

Mulungu wabwino, oyera, osatha—wamuyaya, osasintha
Mulungu ndi ndani?
Osatha wamuyaya
Mulungu wamuyaya wabwino, oyera, osatha osasintha.

sitingamvetse ulemerero wa Mulungu
Wamuyaya osasintha, wosaoneka, Mulungu yekhayo kukhale ulemu, kunthawi zonse.
(1 Timothy 1 ndime 17)
Kukhale ulemu, kunthawi zosatha Amen
Track Name: ANALENGA MULUNGU NDANI?
2. ANALENGA MULUNGU NDANI?

Analenga Mlungu ndani?
Analenga Mlungu ndani?
Palibe anamulenga
Palibe anamulenga
Chorus
Asanabadwe mapiri
Musanalenge dzikoli
Nthawi yosayamba mpaka yosatha
Ndinu Mulungu
(Masalimo 90 ndime 2)
Track Name: KODI MULUNGU ALI NDI CHIYAMBI?
3. KODI MULUNGU ALI NDI CHIYAMBI?

Kodi Mulungu ali ndi chiyambi?
Ayi Mulungu ndi wamuyaya
Woyera woyera Ambuye
Amene analipo, alipo, adzakhalapo

Woyera woyera ,ndi Ambuye
Mulungu wamphamvu
Analipo alipo adzakhalapo
(Chivumbulutso 4 ndime 8)
Track Name: KODI MULUNGU ANGATHE KUFA?
4. KODI MULUNGU ANGATHE KUFA?

Kodi Mulungu angathe kufa?
Ayi ndi wamuyaya
Chorus 1
Kunthawi zanthawi zanthawi zamuyaya
Ndi Mlungu wamoyo ndi mfumu yamuyaya
(yeremiya 10; 10)
Chorus 2
Zaka zanu zikhalira mibadwo mibadwo
Zaka zanu sizifikira kuthaaaa
(Masalimo 102 ndime 24 ndi ndime 27)
Track Name: KODI KULINSO MULUNGU WINA?
5. KODI KULINSO MULUNGU WINA?

Kodi kuli Mulungu wina?
Ayi woona ndi m’modzi
Kodi kuli Mulungu wina
Mulungu ndi m’modzi yekha

Pa Yesaya 45 Mulungu ati
Ine ndine Yehova, popanda Ine palibe Mulungu

Ine ndine Mulungu, palibenso wofananane
Ine ndine Mulungu palibenso

Palibe Mlungu opanda Ine
Idzani kwa Ine mupulumuke
Nonse padziko pakuti
Ndine Mulungu

Wolungama ndi mpulumutsi
Idzani kwaine mupulumuke
Nonse padziko poti
Ndine Mulungu
Track Name: MULUNGU M’MODZI APEZEKA KANGATI?
6. MULUNGU M’MODZI APEZEKA KANGATI?

Mulungu m’modzi apezeka kangati?
Mlungu m’modzi mwa atatu
Mulungu m’modzi apezeka kangati?
Mlungu m’modzi mwa atatu

Chisomo cha Ambuye, Yesu Khristu, Chikondi cha Mulungu ndi Chiyanjano cha Mzimu Woyera chikhale ndi inu nonse
2 Akorinto 13 ndime 14
Chisomo cha mbuye Chikhale nanu
Track Name: MULUNGU MWA ATATU NDI NDANI?
7. MULUNGU MWA ATATU NDI NDANI?

Mulungu mwa atatu ndi ndani?
Mulungu mwatatuyo ndi Atate, Mwana
Mzimu woyera

Mukani phunzitsani anthu onse
Ndi kuwabatiza m’dzina laTate,
Mwana, ndi Mzimu Woyera
(Mateyu 28 ndime 19)
Track Name: MULUNGU ALI KUTI?
8. MULUNGU ALI KUTI?

Ndingapite kuti kuzemba mzimu wanu
Ndithawire kuti kuzemba kupezeka kwanu
Ndingapite m’mwamba, muliko
Ndingakoze kamalanga, pansi, muliko

Mlungu ali ku?
ponsepo
Mlungu ali ku?
Ponsepo

Mulungu ali ponsepo
Ndingakoze kamalanga pansi, muli konko
(Masalimo 139 ndime 7 ndi 8)
Mulungu ali ponseso.
Track Name: MUNGAONE MLUNGU?
9. MUNGAONE MLUNGU?

Mungaone Mlungu?
Ayi, Mulungu ndi Mzimu, ndipo alibe
Thupi ngati munthu
Mungaone Mlungu?
Ngakhale sindimuona
Ndidziwa kuti, andiona nthawi zonse
Ndine Mulungu wapafupi ,si Mlungu wa patali
Ndani munthu angabisale, kuti ine
Ndisamuone? Kodi sindidzala kumwamba ndi pansi
Ati Yehova
Yeremiya 23 ndime 23--24
Track Name: KODI MULUNGU ADZIWA ZONSE?
10. KODI MULUNGU ADZIWA ZONSE?

Kodi Mlungu adziwa zonse?
Inde adziwa zonse
Palibe chobisika kwa Iye

Maso ake ali panjira ya aliyense
Napenya moponda mwake
(Jobu 34:21)

Maso a Mulungu ali ponsepo
Ayang’ana abwino ndi oyipa
(Miyambo 15 ndime 3)
Track Name: KODI MULUNGU ANGATHE ZONSE?
11. KODI MULUNGU ANGATHE ZONSE?

Kodi Mulungu angathe zonse?
Inde chifuniro chake choyera

Ndi Mulungu zonse zotheka
Mateyu 19 ndime 26

Kodi Mulungu angathe zonse
Inde chifuniro chake choyera
Track Name: ANAKULENGA NDANI?
12. ANAKULENGA NDANI?

Anakulenga ndani?
Mulungu
Ndidziwa anandilenga

Pa Genesisi 1 ndime 27 Mau a Mulungu ati
Analenga munthu mchifanizo chake
Mchifanizo chake Mulungu
Analenga mwamuna ndi mkazi
Anakulenga ndani?
Ndidziwa anandilenga
Track Name: ANAKULENGERANJI MULUNGU?
13. ANAKULENGERANJI MULUNGU?

Anakulengeranji Mlungu?
Anakulengeranji Mlungu?
Kodi udziwa?
Anandilenga ndizimulemekeza
Ndikukondwera naye nthawi zonse
Chorus
Mungakhale mudya kapena kumwa
Kaya muchita kanthu kena
Chitani zonse ku ulemerero wa Mulungu
Chorus
Ndingakhale ndidya kapena kumwa
Kaya ndichita kanthu kena
Ndichite zonse ku ulemerero wa Mulungu
( 1 Akorinto 10 ndime 31)
Anandilenga ndizimulemekeza
Track Name: NDI CHANINSO CHOMWE MULUNGU ANALENGA?
14. NDI CHANINSO CHOMWE MULUNGU ANALENGA?

Ndichaninso chomwe
Mulungu analenga?
Mulungu analenga zinthu zonsezi
Chorus
Pachiyambi Mulungu analenga
Kumwamba ndi pansipa
Analenga kuwala usana ndi usiku, thambo ndi Nyanja
Ndi zomera zonse

Kenako chopambana
Analenga munthu
M’chifanizo chake analenga
Mwamuna ndi mkazi
(Genesisi mutu woyamba)
Track Name: MULUNGU ANALENGERANJI ZONSEZI?
15. MULUNGU ANALENGERANJI ZONSEZI?

Mlungu analenganji zonse?
Ulemerero wake
Chifukwa cha ulemerero wake
Analenga zonsezi

Zonse zichokera kwa Iye
Zichitika kufikira kwa Iye
Ulemerero kunthawi zonse

Aroma 11 ndime 36
KwaIye Ulemerero
Kunthawi zonse Amen.
Track Name: UNGATAMANDE BWANJI MLUNGU?
16. UNGATAMANDE BWANJI MLUNGU?

Ungatamande Bwanji Mlungu?
Ndingatamande po mukonda
Ndikuchita zomwe walamula

Wakuonetsa Munthuwe chifundo
Zabwino ndinso Ambuye afuna kwa iwe
kuchitachilungamo
Ndi kukonda chifundo
Kudzichepetsa ndi Mulungu wako
(Mika 6 ndime 8)
Track Name: CHIFUKWA CHANI NDILEMEKEZE MLUNGU?
17. CHIFUKWA CHANI NDILEMEKEZE MLUNGU?

Lemekezani Yehova
Amitundu nonse padziko
Chikondi chake n’chachikulu
Kwa ife
(Masalimo 117)
Chifukwa chiani ndilemekeze Mlungu?
Ndizimulemekeza
Chifukwa chiani ndilemekeze Mlungu
anandilenga
Chifukwa chiani ndilemekeze Mlungu
Andisamalira
Ndilemekeze Mlungu wanga
Track Name: MAKOLO ATHU OYAMBA NDANI?
18. MAKOLO ATHU OYAMBA NDANI?

Makolo oyamba ndani?
Adamu ndi Hava
Adamu ndi Hava ndi makolo oyamba
Chorus
Kenako Mulungu anati
Sibwino munthu akhale yekha
Ndimpangira womuthangatira

Ndipo analenga mkazi napita naye kwa mamuna
Anamutcha Hava m’mayi wa anthu onse
(Genesisi 2 ndi 3)
Track Name: MULUNGU ANAWUMBA BWANJI ADAMU NDI HAVA?
19. MULUNGU ANAWUMBA BWANJI ADAMU NDI HAVA?

Mulungu adawumba bwanji Adamu ndi Hava?
Mulungu anawumba Adamu ndi dothi lapansi,
adawumba bwanji Adamu ndi Hava?
Mulungu anawumba Adamu ndi dothi lapansi,
Napanga Hava ku mthiti ya Adamu
Genesisi 2 ndime 7
anawumba munghu ndi dothi la pansi
Genesisi 2 ndime 22
napanga mkazi ku mthiti ya mamuna
Track Name: ANAPEREKA CHIANI MULUNGU KWA ADAMU NDI HAVA PAMWAMBA PA THUPI?
20. ANAPEREKA CHIANI MULUNGU KWA ADAMU NDI HAVA PAMWAMBA PA THUPI? 

Anapereka chiani kwa Adamu ndi Hava pamwamba pa thupi?
Mulungu anawapatsa mzimu womwe sudzafa
Anapereka chiani kwa Adamu ndi Hava pamwamba pa thupi?
Mulungu anawapatsa mzimu womwe sudzafa

Ambuye anapanga muthu kuchoker ku dothi lapansi
Nauzira munthuo mpweya wa moyo
Ndipo munthu anakhala wamoyo
Mulungu anamuuzira mpweya wa moyo
Genesisi 2 ndime 7
Mulungu anamuuzira mpweya wa moyo
Track Name: KODI ULI NDI MZIMU NDIPONSO THUPI?
21. KODI ULI NDI MZIMU NDIPONSO THUPI?

Kodi uli ndi mzimu ndiponso thupi?
Inde mzimu womwe sudzafa
Kodi uli ndi mzimu ndiponso thupi?
Inde mzimu womwe sudzafa
Mlaliki 12 ndime 7
Fumbi ku fumbi
Mzimu kubwerera kwa Mulungu anaupereka
Track Name: KODI ADAMU NDI HAVA MULUNGU ANAWALENGA OTANI?
22. KODI ADAMU NDI HAVA MULUNGU ANAWALENGA OTANI?

Kodi Adamu ndi Hava
Mulungu anawalenga otani?
Anawalenga amgwiro ndi okondwa

Genesis 2 ndime 25
Onse anali okondwa
Genesis 2 ndime 25
Anali okondwa opanda manyazi